Ezekiel 41:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adayesa kutalika kwa nyumba yoyang'anana ndi bwalolo chakuzambwe kwa Nyumba ya Mulungu, ndi njira zam'kati ku mbali iliyonse. Zonsezo zinali za mamita makumi asanu. Chipinda cha m'thunthu mwa Nyumba ya Mulungu, chipinda cham'kati ndiponso khonde lam'kati loyang'ana kunja,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo anayesa m'litali mwake nyumbayo inali kutsogolo kwake kwa mpata wokhala chakuno chake, ndi makonde ake am'mwamba, chakuno ndi chauko, mikono zana limodzi, ndi Kachisi wa m'katimo, ndi makonde a kubwalo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anayeza kutalika kwa nyumba yoyangʼanana ndi bwalo chakumadzulo kwa Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo njira zamʼkati ku mbali iliyonse. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu. Chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, chimene chili chamʼkati, khonde lamʼkati loyangʼanana ndi bwalo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo anayesa m'litali mwace nyumbayo inali kutsogolo kwace kwa mpata wokhala cakuno cace, ndi makonde ace am'mwamba, cakuno ndi cauko, mikono zana limodzi, ndi Kacisi wa m'katimo, ndi makonde a kubwalo;