Ezekiel 41:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mazenera ndi made ake, zonsezo zinali zochingidwa ndi matabwa. Pamwamba, kupenyana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu idaakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, ndipo mazenerawo anali okutidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ziundo, ndi mazenera amkati okhazikika, ndi makonde am'mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa chiundo, otchinga ndi matabwa pozungulira pake, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mazenera ndi maferemu ake, zonsezi zinali zokutidwa ndi matabwa. Pamwamba moyangʼanana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu inakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, (mazenerawo anali okutidwa),
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ziundo, ndi mazenera a made okhazikika, ndi makonde am'mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa ciundo, ocinga ndi matabwa pozungulira pace, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika;