Ezekiel 41:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ina inali nkhope ya munthu, yoyang'ana kanjedza wa mbali imodzi, ina inali nkhope ya mkango yoyang'ana kanjedza wa mbali ina. Zidachingidwa choncho kuzungulira Nyumba yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nkhope ya munthu kuloza kukanjedza chakuno, ndi nkhope ya mwanawamkango kuloza kukanjedza chauko, momwemo m'nyumba monse pozungulira pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
imodzi inali nkhope ya munthu yoyangʼana kanjedza mbali imodzi, ndi ina inali nkhope ya mkango yoyangʼana kanjedza mbali ina. Zinajambulidwa kuzungulira Nyumba ya Mulungu yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nkhope ya munthu kuloza kukanjedza cakuno, ndi nkhope ya mwana wa mkango kuloza kukanjedza cauko, momwemo m'nyumba monse pozungulira pace.