Ezekiel 41:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muufupi mwake mwa khomo munali mamita asanu. Zipupa zake zam'mbali zinali za mamita aŵiri ndi theka muufupi mwake mbali iliyonse. Adayesa kutalika kwake kwa chipindacho, kunali mamita makumi aŵiri, muufupi mwake mamita khumi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; nayesa malo opatulika, m'litali mwake mikono makumi anai, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulifupi mwa khomo munali motalika mamita asanu. Makoma a mbali zonse anali a mamita awiri ndi theka mulifupi mwake. Anayezanso kutalika kwa chipinda chopatulika chija ndipo mulitali mwake munali motalika mamita makumi awiri ndi mulifupi mwake munali mamita khumi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu cakuno, ndi mikono isanu cauko; nayesa malo opatulika, m'litali mwace mikono makumi anai, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri.