Ezekiel 41:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa zitseko panali zithunzi zozokota za akerubi ndi za kanjedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kachisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo komanso pa makoma onse a chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, anajambula zithunzi za akerubi ndi kanjedza pa makoma onse a malo opatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kacisi.