Ezekiel 41:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali wa mita limodzi ndi hafu, m'litali mwake munali mita limodzi, muufupi mwake munalinso mita limodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi makoma ake, zonse zinali zopanga ndi mtengo. Munthu uja adandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limene limakhala pamaso pa Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m'litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka, mulitali mwake munali mita imodzi, mulifupi mwake munalinso mita imodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi mbali zonse zinali za matabwa. Munthuyo anandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limakhala pamaso pa Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wace mikono itatu, ndi m'litali mwace mikono iwiri, ndi ngondya zace, ndi tsinde lace, ndi: thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome liri pamaso pa Yehova.