Ezekiel 41:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa mbali zonse za khonde lam'katilo panali mazenera, ndipo pa zipupa zake zonse adazokotapo zithunzi za kanjedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali mazenera amkati okhazikika, ndi akanjedza chakuno ndi chauko, kumbali zake za khonde; momwemonso pa zipinda za m'mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ochindikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mbali zonse za khonde lamʼkatilo panali mazenera, ndipo pa makoma ake onse anajambulapo zithunzi za kanjedza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali mazenera a made okhazikika, ndi akanjedza cakuno ndi cauko, kumbali zace za khonde; momwemonso pa zipinda za m'mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ocindikira.