Ezekiel 41:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adakaloŵa m'kati nakayesa mphuthu zapakhomo. Zinali za mita limodzi, ndipo khomolo linali la mamita atatu. Zipupa za m'mbali mwa khomolo zinali za mamita atatu ndi theka mbali iliyonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalowa m'katimo, nayesa mphuthu za pakhomo mikono iwiri, ndi msinkhu wa khomo mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwa khomo mikono isanu ndi iwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka munthuyo anakalowa mʼkati ndipo anayeza khonde la pa khomo; khondelo linali mita imodzi mulifupi mwake. Mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalowa m'katimo, nayesa mphuthu za pakhomo mikono iwiri, ndi msinkhu wa khomo mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwa khomo mikono isanu ndi iwiri.