Ezekiel 41:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adayesa chipinda chenichenicho napeza kuti m'litali mwake ndi muufupi mwake munali mamita khumi. Apo adandiwuza kuti, “Chimenechi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anayesanso m'kati mwa Kachisi m'tsogolomo, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m'mopatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso anayeza kutalika kwa chipinda chopatulika chenichenicho. Mulitali mwake munali mamita khumi, ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi. Munthuyo anandiwuza kuti, “Ichi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anayesanso m'kati mwa Kacisi m'tsogolomo, m'litali mwace mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m'mopatulikitsa.