Ezekiel 41:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthu uja adayesa khoma la Nyumba ya Mulungu, linali la mamita atatu. Panali zipinda zina kuzungulira Nyumbayo, chilichonse muufupi mwake chinali cha mamita aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anayesa khoma la nyumba, kuchindikira kwake mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwake kwa zipinda za m'mphepete mikono inai, pozungulira pake ponse pa Kachisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono munthuyo anayeza khoma la Nyumba ya Mulungu; kuchindikira kwake kunali mamita atatu. Panalinso zipinda zina kuzungulira Nyumba ya Mulungu ndipo chilichonse chinali cha mamita awiri mulifupi wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anayesa khoma la nyumba, kucindikira kwace mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwace kwa zipinda za m'mphepete mikono inai, pozungulira pace ponse pa kacisi.