Ezekiel 41:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana, chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulunguyo panali zochirikiza zipindazo, kuti zisamatsamire pa chipupa cha Nyumba ya Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zipinda za m'mphepete zinasanjikizana china pa chinzake; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, nizinalowa kukhoma lochirikiza zipinda za m'mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwa ndi khoma la nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana. Chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulungu panali zochirikiza zipindazo kuti zisatsamire khoma la Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zipinda za m'mphepete zinasanjikizana cina pa cinzace; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, nizinalowa ku khoma locirikiza zipinda za m'mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwa ndi khoma la nyumba.