Ezekiel 41:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipinda zam'mbalizo zinkapita zikukulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda, potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika chapamwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zipinda za m'mphepete zinakula m'kupingasa kwao, pozinga nyumba m'kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pake pa nyumba; motero kupingasa kwake kwa nyumba kunakula kumwamba kwake, momwemonso anakwera kuyambira chipinda chakunsi, kupita chapakati, kufikira cham'mwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipinda za mʼmbalizo zinkapita zikulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika pamwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zipinda za m'mphepete zinakula m'kupingasa kwao, pozinga nyumba m'kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pace pa nyumba; motero kupingasa kwace kwa nyumba kunakula kumwamba kwace, momwemonso anakwera kuyambira cipinda cakunsi, kupita capakati, kufikira cam'mwamba.