Ezekiel 41:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidaona chiwundo chozungulira Nyumba ya Mulungu. Chidapanga maziko a zipindazo, ndipo chinali cha mamita atatu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinaonanso kuti kunyumba kunali chiunda pozungulira pake; maziko a zipinda za m'mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinaona chiwundo kuzungulira Nyumba ya Mulungu. Chinapanga maziko a zipindazo ndipo chinali cha mamita atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinaonanso kuti kunyumba kunali ciunda pozungulira pace; maziko a zipinda za m'mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikuru.