Ezekiel 42:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake munthu uja adapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto, nandiloŵetsa m'nyumba ina yoyang'anana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anatuluka nane kunka kubwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane kunyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto ndipo anafika nane ku zipinda zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaturuka nane kumka ku bwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane ku nyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.