Ezekiel 42:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbali yakumwera, kuyang'anana ndi bwalo ndi nyumbayo, kunali zipinda zina, ndipo kumaso kwake kunali njira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'kuchindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, chakuno cha mpatawo, chakuno cha nyumba, panali nyumba yazipinda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbali yakummwera kuyangʼanana ndi bwalo ndi nyumbayo kunali zipinda zina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'kucindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, cakuno ca mpatawo, cakuno ca nyumba, panali nyumba yazipinda.