Ezekiel 42:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipinda zimenezi m'litali mwake ndi muufupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zolingana ndi zoyang'ana kumpoto zija. Makomo ake ndi zitseko zake zinalinso zolingana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe njira ya kunyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m'litali mwake, momwemonso kupingasa kwake; ndi m'matulukiro mwake monse munali monga mwa machitidwe a inzake, ndi monga mwa makomo a inzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumaso kwa zipindazi kunali njira. Zipindazi mulitali mwake, mulifupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zofanana ndi zipinda zoyangʼana zakumpoto zija. Makomo ndi zitseko zake zinalinso zofanana
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe a njira ya ku nyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m'litali mwace, momwemonso kupingasa kwace; ndi m'maturukiro mwace monse munali monga mwa macitidwe a inzace, ndi monga mwa makomo a inzace.