Ezekiel 42:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthu uja adandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakumwera zoyang'anana ndi khonde nzoyera. M'menemo ansembe okhala kufupi ndi Chauta amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. M'menemo adzaikamo zopereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za chakudya, nsembe yopepesera machimo, ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi oyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo munthuyo anandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakummwera zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi zoyera. Mʼmenemo ansembe amene amakhala pafupi ndi Yehova amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. Mʼmenemo adzayikamo zopereka zopatulika kwambiri, zopereka za chakudya, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi opatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwela, ziri cakuno ca mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulikitsa; kumeneko aziika zopatulikitsa, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula; pakuti malowo ndi opatulika.