Ezekiel 42:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe ataloŵa m'malo oyerawo, sadzatulukamo kupita m'bwalo lakunja popanda kusiya m'menemo zovala zimene amavala potumikira zija. Zimenezi nzoyera. Ayenera kuvala zina asanafike pa anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atalowa ansembe asatulukenso m'malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ansembe alowa ku malo opatulikawa, asatuluke kupita ku bwalo lakunja popanda kusiya momwemo zovala zimene anavala potumikira zija, pakuti zovalazi ndi zopatulika. Avale kaye zovala zina ndipo akhoza kufika kwa anthu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atalowa ansembe asaturukenso m'malo opatulika kumka ku bwalo lakunja, koma komweko aziika zobvala zao zimene atumikira nazo; pakuti ziri zopatulika; ndipo abvale zobvala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.