Ezekiel 42:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamaliza kuyesa m'kati mwa Nyumba ya Mulungu, munthu uja adatuluka nane pa chipata chopenya kuvuma. Pamenepo adayesa bwalo lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anatuluka nane njira ya chipata choloza kum'mawa nayesa bwalo pozungulira pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo atamaliza kuyeza zimene zinali mʼkati mwa Nyumba ya Mulungu, anatuluka nane pa chipata chakummawa ndi kuyeza bwalo lonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anaturuka nane njira ya cipata coloza kum'mawa, nayesa bwalo pozungulira pace.