Ezekiel 42:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyang'anana ndi bwalo lam'kati la mamita khumi, ndiponso kuyang'anana ndi chiwundo cha bwalo lakunja, panali makonde atatu osanjikana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzake losanjikika pachiwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panali midadada iwiri, umodzi umayangʼanana ndi bwalo lamʼkati la mamita khumi, winawo umayangʼanana ndi bwalo lakunja. Midadada iwiriyi inali ya nyumba zitatu zosanjikana ndipo imayangʼanana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzace losanjikika paciwiri.