Ezekiel 42:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipinda zam'mwamba zinali zazifupi m'mimbamu kupambana zam'munsi ndi zapakati, chifukwa njira zake zam'kati zidaalanda malo ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zipinda zapamwamba zinachepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, chifukwa chake zinachepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipinda zammwamba zinali zazifupi mʼmimbamu kupambana zipinda zamʼmunsi ndi zipinda zapakati chifukwa njira zake zinatenga malo ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zipinda zapamwamba zinacepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, cifukwa cace zinacepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda.