Ezekiel 42:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Khoma lakunja, kutalika kwake mamita 25, linkatsatana ndi zipinda kutsogolo kwake pambali pa bwalo lakunja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo linga linali kunjalo, lolingana ndi nyumba yazipinda, kuloza kubwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwake munali mikono makumi asanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Panali khoma lakunja lomwe limatsatana ndi zipindazo kutsogolo kwake pambali pabwalo lakunja, kutalika kwake kunali mamita 25.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo linga linali kunialo, loli'ngana ndi nyumba yazipinda, kuloza ku bwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwace munali mikono makumi asanu.