Ezekiel 42:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zipinda za m'mbali mwa bwalo lakunja m'litali mwake zinali za mamita 25. Koma zokhala m'mbali mwa Nyumba ya Mulungu ija m'litali mwake zinali za mamita makumi asanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kupingasa kwake kwa nyumba yazipinda inali m'bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza kukhomo la Kachisi inali mikono zana limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zipinda za mʼmbali mwa bwalo lakunja mulitali mwake munali mamita 25. Koma zomwe zinali mʼmbali mwa Nyumba ya Mulungu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kupingasa kwace kwa nyumba yazipinda inali m'bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza ku khomo la Kacisi inali mikono zana limodzi.