Ezekiel 43:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akachita manyazi ndi zoipa zonse zimene adachita, uŵasimbire za Nyumba ya Mulungu ndi maonekedwe ake, za makomo ake otulukira ndi oloŵera, za kaonekedwe kake konse ndi za makonzedwe ake onse. Uŵafotokozere malamulo ndi malangizo ake, ndipo uŵalembe iwo akuwona, kuti aziŵakumbukira ndi kumaŵatsatadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati akachita manyazi nazo zonse anazichita, uwadziwitse maonekedwe a Kachisiyu, ndi muyeso wake, ndi potulukira pake, ndi polowera pake, ndi malongosoledwe ake onse, ndi malemba ake onse, ngakhale maonekedwe ake onse, ndi malamulo ake onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ake onse, ndi malemba ake onse, nawachite.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
akachita manyazi ndi zoyipa zonse anachita, uwafotokozera za Nyumba ya Mulungu, mamangidwe ake, makomo ake otulukira ndi makomo olowera, ndiye kuti, mamangidwe ake onse. Uwafotokozerenso malangizo ndi malamulo ake. Uwalembe akuona kuti athe kuwasunga ndi kuwachita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati akacita manyazi nazo zonse anazicita, uwadziwitse maonekedwe a kacisiyu, ndi muyeso wace, ndi poturukira pace, ndi polowera pace, ndi malongosoledwe ace onse, ndi malemba ace onse, ngakhale maonekedwe ace onse, ndi malamulo ace onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ace onse, ndi malemba ace onse, nawacite.