Ezekiel 43:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nayi miyeso ya guwa lansembe potsata miyeso yomwe ija imene adaayesera Nyumba ya Mulungu. Patsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake, ndiponso muufupi mwake. M'milomo mwake mwa ngalandeyo mudzakhala mwa mjintchi wa masentimita 25.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi chikhato), tsinde lake likhale mkono, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, ndi mkuzi wake m'mphepete mwake pozungulira pake kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Miyeso ya guwa lansembe ndi iyi: Pa tsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake ndi mulifupi mwake. Mʼphepete mwa ngalandeyo kuzungulira guwa lonse, mudzakhala mkombero wa masentimita 25.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi cikhato), tsinde lace likhale mkono, ndi kupingasa kwace mkono, ndi mkuzi wace m'mphepete mwace pozungulira pace kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali.