Ezekiel 43:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Guwalo msinkhu wake udzakhala wotere: kuchokera pa tsinde pansi mpaka pa phaka lapansi mita limodzi, muufupi mwake theka la mita. Kuchokera ku phaka laling'ono mpaka ku phaka lalikulu, msinkhu wake udzakhala mamita aŵiri, muufupi mwake mudzakhala masentimita makumi asanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kuyambira kunsi kwake kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwake mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikulu mikono inai; ndi kupingasa kwake mkono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera mʼngalande ya pansi padzakhala mpaka pa phaka lapansi mita imodzi, mulifupi mwake theka la mita. Kuchokera pa phaka lalingʼono mpaka pa phaka lalikulu, msinkhu wake ndi mamita awiri, mulifupi mwake ndi masentimita makumi asanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kuyambira kunsi kwace kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwace mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikuru mikono inai; ndi kupingasa kwace mkono.