Ezekiel 43:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Phaka lapakati lidzakhala la mamita asanu ndi aŵiri kutalika kwake, ndiponso asanu ndi aŵiri muufupi mwake, pa mbali zake zonse zinai. Ndipo mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 mjintchi wake. Ngalande ya patsinde pa guwalo idzakhala ya masentimita makumi asanu, ndipo makwerero a paguwapo adzayang'ana kuvuma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi phaka, m'litali mwake mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi inai kumbali zake zinai; ndi mkuzi wake pozungulira pake mkono wa nusu, ndi tsinde lake mkono pozungulira pake, ndi makwerero ake aloza kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Phaka lapamwamba muyeso wake udzakhala wofanana mbali zonse. Mulitali mudzakhala mamita asanu ndi awiri ndiponso mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi awiri. Mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 ndiponso ngalande yake yozungulira idzakhala ya masentimita 25. Makwerero a guwa lansembe adzayangʼana kummawa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi phaka, m'litali mwace mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwace mikono khumi ndi inai ku mbali zace zinai; ndi mkuzi wace pozungulira pace mkono wa nusu, ndi tsinde lace mkono pozungulira pace, ndi makwerero ace aloza kum'mawa.