Ezekiel 43:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe a fuko la Levi, am'banja la Zadoki, ndiwo azibwera pafupi nane kudzanditumikira. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Udzaŵapatse mwanawang'ombe wamphongo kuti aperekere nsembe yopepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Upatse ansembe Alevi, a mbeu za Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwanawang'ombe, akhale wa nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzawapatse ansembe, omwe ndi Alevi, a banja la Zadoki, amene amabwera pafupi nane kudzanditumikira, mwana wangʼombe wamwamuna kuti aperekere nsembe yopepesera machimo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Upatse ansembe Alevi, a mbeu ya Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwana wa ng'ombe, akhale wa nsembe yaucimo.