Ezekiel 43:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Utaipha, udzatengeko magazi, ndi kuŵapaka pa nyanga zinai za guwa pa ngodya zinai za phaka, ndiponso kuzungulira mkombero. Motero udzaliyeretsa guwalo ndi kulidalitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzatengeko magazi ake ena ndi kuwapaka pa nyanga zinayi za pa guwa lansembe, pa ngodya zinayi za phaka ndiponso mozungulira mkombero wonse. Motero udzaliyeretsa ndi kulipatula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nutengeko mwazi wace, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pa ngondya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wace pozungulira; motero uliyeretse ndi kulicitira cotetezera.