Ezekiel 43:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka udzatenge ng'ombe yamphongo imene yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo. Udzaitenthe pa malo ake enieni, m'bwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Utengenso ng'ombe ya nsembe yauchimo, aipsereze pa malo oikika a Kachisi kunja kwa malo opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzatenge ngʼombe yayimuna yomwe yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo, ndipo udzayiwotche pa malo ake enieni mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Utengenso ng'ombe ya nsembe yaucimo, aipsereze pa malo oikika a kacisi kunja kwa malo opatulika.