Ezekiel 43:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake udzapereke tonde wopanda chilema, kuti nayenso akhale nsembe yopepesera machimo. Ndi tondeyo udzayeretse guwalo monga momwe udachitira ndi ng'ombe yamphongo ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lachiwiri upereke tonde wopanda chilema, akhale nsembe yauchimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mmawa mwake udzatenge mbuzi yopanda chilema kuti nayonso iperekedwe ngati nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake idzayeretse guwa lansembe monga unachitira ndi ngʼombe yayimuna ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku laciwiri upereke tonde wopanda cirema, akhale nsembe yaucimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo.