Ezekiel 43:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lililonse pa masiku asanu ndi aŵiri uzidzapereka tonde, ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo, kuperekera nsembe yopepesera machimo. Zonsezo zidzakhale zopanda chilema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yauchimo; akonzerenso mwanawang'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda chilema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kwa masiku asanu ndi awiri, uzidzapereka tsiku ndi tsiku mbuzi yayimuna, mwana wangʼombe, ndiponso nkhosa kuti zikhale nsembe zopepesera machimo. Zonsezi zidzakhale zopanda chilema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yaucimo; akonzerenso mwana wa ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda cirema.