Ezekiel 43:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene ndidaziwona m'masomphenya zinali ngati zomwe ndidaaziwona zija pamene Chauta adaabwera kudzaononga mzinda. Zinalinso ngati zimene ndidaaziwona ku mtsinje wa Kebara. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona kumtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masomphenya amene ndinawaonawa anali ngati masomphenya amene ndinawaona pamene Yehova anabwera kudzawononga mzinda ndiponso ngati masomphenya amene ndinawaona ku mtsinje wa Kebara. Ndipo ndinadzigwetsa chafufumimba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona ku mtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi.