Ezekiel 43:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, malo ano ndi malo a mpando wanga waufumu, malo amene ndimapondapo mapazi anga. Kuno ndiye kumene ndidzakhale pakati pa anthu anga Aisraele mpaka muyaya. Iwowo ngakhalenso mafumu ao, sadzaipitsanso dzina langa loyera pokhala osakhulupirika kapena poika mitembo ya mafumu ao ku zitunda zachipembedzo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga waufumu, ndi malo opondapo mapazi anga. Pano ndiye pamene ndidzakhala pakati pa Aisraeli mpaka muyaya. Aisraeliwa kapena mafumu awo sadzayipitsa dzina langa popembedza milungu ina kapena poyika mitembo ya mafumu awo ku zitunda zachipembedzo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wacifumu wanga, mpoponda ku mapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israyeli kosatha; ndi nyumba ya Israyeli siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa cigololo cao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,