Ezekiel 43:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankamanga chiwundo chao pafupi ndi changa ndiponso mphuthu zao pafupi ndi zanga, nkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero ankaipitsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao zimene ankachita. Tsono ndidaŵaononga ndili wokwiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuika chiundo chao pafupi pa chiundo changa, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazichita; chifukwa chake ndinawatha mu mkwiyo wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankamanga chiwundo chawo pafupi ndi chiwundo changa, ndiponso mphuthu zawo pafupi ndi mphuthu zanga, nʼkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero anayipitsa dzina langa loyera ndi machitidwe awo onyansa. Choncho Ine ndinawawononga ndili wokwiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuika ciundo cao pafupi pa ciundo canga, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazicita; cifukwa cace ndinawatha mu mkwiyo wanga.