Ezekiel 44:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono Alevi amene adaandisiya kutali pa nthaŵi imene Aisraele adaasokera potsata mafano, adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Aleviwo anandichokera kunka kutaliwo, posokera Israele, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndiponso Alevi amene anandisiya kutali pa nthawi imene Israeli anasochera potsata mafano, adzalangidwa chifukwa cha tchimo lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Aleviwo anandicokera kumka kutariwo, posokera Israyeli, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao.