Ezekiel 44:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzangokhala atumiki chabe ku malo anga opatulika. Adzayang'anira zipata za Nyumba ya Mulungu ndi kugwira ntchito zina zake kumeneko. Adzapha nyama za nsembe zopsereza, ndi za nsembe zina za anthu. Motero adzidzaimirira anthuwo ndi kumaŵatumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira kuzipata za Kachisi, ndi kutumikira m'Kachisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera, naime pamaso pao kuwatumikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzangokhala atumiki chabe mʼmalo anga opatulika. Azidzayangʼanira zipata za Nyumba ya Mulungu ndi kugwira ntchito kumeneko. Azidzapha nyama za nsembe zopsereza ndi za nsembe zina za anthu. Choncho azidzayimirira pamaso pa anthu nʼkumawatumikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira ku zipata za kacisi, ndi kutumikira m'kacisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera naime pamaso pao kuwatumikira.