Ezekiel 44:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo ankatumikira anthu popembedza mafano, ndipo adasokeretsa Aisraele potero. Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikulumbira ndithu kuti ameneŵa ayenera kulangidwa chifukwa cha zolakwa zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala chokhumudwitsa cha mphulupulu cha nyumba ya Israele, chifukwa chake ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwowa ankatumikira anthu popembedza mafano awo, ndipo anachititsa Aisraeli kugwa mu uchimo. Nʼchifukwa chake Ine ndikulumbira kuti iwowa ayenera kulangidwa chifukwa cha machimo awo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala cokhumudwitsa ca mphulupulu ca nyumba ya Israyeli, cifukwa cace ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao.