Ezekiel 44:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saloledwa kudzafika pafupi ndi Ine, kuti anditumikire ngati ansembe. Sadzayandikira zinthu zanga zopatulika ndi zopereka zoyera kwambiri. Adzachititsidwa manyazi chifukwa cha ntchito zao zonyansa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira ntchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga zilizonse zopatulika kwambirizo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazichita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo sayenera kufika pafupi ndi Ine ndi kunditumikira ngati ansembe, kapena kuyandikira chilichonse cha zinthu zanga zopatulika, kapenanso zopereka zanga zopatulika kwambiri. Iwo adzachititsidwa manyazi chifukwa cha machitidwe awo onyansa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira nchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga ziri zonse zopatulikitsazo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazicita.