Ezekiel 44:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma ansembe a fuko la Levi a m'banja la Zadoki, amene adakhalabe okhulupirika pa ntchito zosamala malo anga opatulika nthaŵi imene Aisraele adaasokera ndi kundisiya Ine, okhawo adzasendera kwa Ine kuti anditumikire. Adzabwera kwa Ine kudzapereka nsembe za mafuta ndi magazi. Ndatero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma ansembe, a fuko la Levi, a banja la Zadoki amene ankatumikira mokhulupirika ku malo anga opatulika pa nthawi imene Aisraeli anasochera ndi kundisiya Ine; iwowa adzasendera kwa Ine kudzanditumikira. Adzafika pamaso panga kuti apereke nsembe za mafuta ndi magazi. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israyeli, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;