Ezekiel 44:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene aloŵa ku chipata cham'kati, azivala bafuta. Asavale chovala chilichonse cha ubweya wankhosa ponditumikira pa zipata za bwalo lam'kati ndiponso m'kati mwa Nyumba yanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzatero, polowa iwo kuzipata za bwalo lam'kati avale zovala zabafuta; koma zaubweya asazivale ponditumikira Ine m'zipata za bwalo la m'kati, ndi m'Kachisi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene alowa ku zipata za bwalo lamʼkati azivala zovala zabafuta. Asamavale chovala china chilichonse cha ubweya wankhosa pamene akutumikira pa zipata za bwalo la mʼkati kapena kunja kwa Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzatero, polowa iwo ku zipata za bwalo lam'kati abvale zobvala zabafuta; koma zaubweya asazibvale ponditumikira Ine m'zipata za bwalo la m'kati, ndi m'kacisi.