Ezekiel 44:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Potulukira ku anthu a ku bwalo lakunja, azivula zovala zimene anavala potumikira m'kati, ndi kuzisiya m'zipinda zopatulika. Ndipo avale zovala zina, kuwopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo ndi zovala zaozo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akatulukira kubwalo lakunja, kubwalo lakunja kuli anthu, azivula zovala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, navale zovala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene atuluka ndi kupita ku bwalo lakunja kumene kuli anthu, azivula zovala zimene amatumikira nazo, ndipo azisiye zovalazo mu zipinda zopatulika. Pambuyo pake avale zovala zina, kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo ndi zovala zawozo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akaturukira ku bwalo lakunja, ku bwalo lakunja kuti anthu, azibvula zobvala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, nabvale zobvala zina; angapatule anthu ndi zovala zao.