Ezekiel 44:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asakwatire mkazi wamasiye wamba kapena mkazi wosudzulidwa. Azikwatira namwali wosadziŵa mwamuna, ŵa fuko la Israele, kapena mkazi wamasiye wa wansembe mnzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asachite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israele, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo asakwatire akazi amasiye kapena osudzulidwa; koma azikwatira anamwali osadziwa mwamuna a fuko la Israeli kapena akazi amasiye a ansembe anzawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asacite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israyeli, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe.