Ezekiel 44:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakakhala milandu, ansembe adzakhala oweruza, ndipo adzayenera kugamula milanduyo potsata malamulo anga. Atsate malamulo anga ndi malangizo anga pa za masiku anga onse achikondwerero. Adzasamalenso kuti masiku anga a Sabata akhale oyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pazikondwerero zanga zonse zoikika; napatulikitse masabata anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pakakhala milandu, ansembe azikhala oweruza ndipo agamule milanduyo potsata malamulo anga. Atsate malamulo anga ndi malangizo anga pa za masiku anga onse a chikondwerero. Asamalirenso kuti masiku anga a Sabata akhale oyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pa madyerero anga onse oikika; napatulikitse masabata anga.