Ezekiel 44:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Wansembe asadziipitse pokhudza munthu wakufa, kupatula ngati ndi bambo wake kapena mai wake, mwana wake wamwamuna kapena wamkazi, mbale wake kapena mlongo wake wosakwatiwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo asayandikire kwa munthu aliyense wakufa, angadzidetse; koma chifukwa cha atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Wansembe asadziyipitse pokhudza munthu wakufa, pokhapokha ngati wakufayo ndi abambo ake kapena amayi ake, mwana wake wamwamuna kapena wamkazi, mʼbale wake kapena mlongo wake wosakwatiwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo asayandikire kwa munthu ali yense wakufa, angadzidetse; koma cifukwa ca atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa.