Ezekiel 44:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo azidzadyako za chopereka cha zakudya, za nsembe zopepesera machimo, ndi za nsembe zopepesera kupalamula. Ndipo zonse zoperekedwa kwa Mulungu mu Israele zidzakhala zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere m'Israele ndi zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo azidzadya nsembe ya chakudya, nsembe yopereka chifukwa cha tchimo ndi nsembe yopepesera machimo. Zinthu zonse zoperekedwa kwa Yehova mu Israeli zidzakhala zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula; ndipo ziri zonse zoperekedwa ciperekere m'Israyeli ndi zao.