Ezekiel 44:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zopambana pa zonse zoyambirira kucha ndi pa zopereka zina zonse, zidzakhale za ansembe. Muzidzaŵapatsa ufa wanu umene mwayambirira kusinja, kuti choncho m'nyumba mwanu mukhale madalitso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zabwino za zipatso zanu zoyambirira kucha ndiponso mphatso zanu zonse zapadera zidzakhala za ansembe. Inu muziwapatsa chigawo choyamba cha ufa wanu kuti pa nyumba panu pakhale madalitso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu ziri zonse, ndi nsembe za kweza ziri zonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako.