Ezekiel 44:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake munthuyo adandidzeretsa pa chipata chakumpoto ndipo tidafika kumaso kwa Nyumba ya Mulungu. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Chauta utadzaza Nyumba yakeyo. Pamenepo ndidadzigwetsa chafufumimba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atatero anamuka nane njira ya chipata cha kumpoto kukhomo kwa Kachisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka munthuyo anandidzeretsa pa chipata chakumpoto ndipo tinafika kumaso kwa Nyumba ya Mulungu. Nditapenyetsetsa ndinangoona ulemerero wa Yehova utadzaza mʼNyumba ya Mulungu, ndipo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atatero anamuka nane njira ya cipata ca kumpoto kukhomo kwa kacisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi.