Ezekiel 44:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, samala bwino, uyang'anitsitse ndipo umvetse bwino zonse zimene ndikuuze za malamulo ndi malangizo okhudza za Nyumba yangayi. Uzindikire bwino amene angaloledwe kuloŵa m'Nyumba ino ndiponso amene sayenera kuloŵamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ake onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi matulukidwe ake onse a malo opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, samala bwino ndipo uyangʼanitsitse ndi kumvetsa bwino zonse zimene ndikuwuze zokhudza malamulo ndi malangizo a Nyumbayi. Usamalitse za amene angalowe ndi kutuluka mʼNyumbayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ace onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi maturukidwe ace onse a malo opatulika.