Ezekiel 44:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudaloŵetsa m'malo anga opatulika alendo osaumbalidwa mu mtima ndi m'thupi momwe. Anthuwo adaipitsa Nyumba yanga pamene inu munkandipatsa chakudya, mafuta ndi magazi omwe. Pochita zoipa zoterezi mudaphwanya chipangano changa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munalowetsa alendo osachita mdulidwe mu mtima ndi mʼthupi momwe mʼNyumba yanga ndipotu anayipitsa Nyumba yanga. Pamene inu munkandipatsa chakudya changa ndi magazi omwe kuwonjezera pa zonyansa zanu zonse ndiye kuti munaphwanya pangano langa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza mwalowa nao acilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munatyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.